2 Samuel 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu mapiri a ku Gilibowa, pa inu pasagwe mame ndi mvula, pa inu pasapezeke minda yobereka dzinthu. Paja kumeneko adani adanyoza chishango cha munthu wamphamvu, chishango cha Saulo, chosapukutidwapo ndi mafuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu mapiri a ku Gilibowa, musakhalenso ndi mame kapena mvula, kapena minda yobereka zopereka za ufa. Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa, chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mapiri inu a Giliboa, Pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, Cikopa ca Sauli, monga ca wosadzozedwa ndi mafuta.