2 Samuel 1:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uta wa Yonatani sudabwereko chabe osakhetsa magazi a anthu osabayako ankhondo amphamvu. Ndipo lupanga la Saulo silidabwereko chabe osapha anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uta wa Yonatani sunabwerera, ndipo lupanga la Saulo silinabwerera chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa magazi a ophedwa, pa mnofu wa amphamvu, uta wa Yonatani sunabwerere, lupanga la Sauli silinabwere chabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uta wa Jonatani sunabwerera, Ndipo lupanga la Sauli silinabwecera cabe, Pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.