2 Samuel 1:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Saulo ndi Yonatani pa moyo wao anali okondedwa ndi okondwetsa, ndipo sadalekane ali moyo ngakhale pa imfa. Anali ndi liŵiro loposa la ziwombankhanga. Anali amphamvu kuposa mikango.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo m'imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Sauli ndi Yonatani, pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima, ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe. Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga, anali ndi mphamvu zoposa mkango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sauli ndi Jonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, Ndipo m'imfa yao sanasiyana; Anali nalo liwiro loposa ciombankanga, Anali amphamvu koposa mikango.