2 Samuel 1:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mbale wanga Yonatani, ndikuvutika mu mtima chifukwa cha iwe, wakhala wapamtima wanga. Chikondi chako pa ine chinali chodabwitsa kwambiri, chinali choposa ngakhale chikondi cha akazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani, unali wokondedwa kwambiri kwa ine. Chikondi chako pa ine chinali chopambana, chopambana kuposa chikondi cha akazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipsinjika mtima cifukwa ca iwe, mbale wanga Jonatani; Wandikomera kwambiri; Cikondi cako, ndinadabwa naco, Cinaposa cikondi ca anthu akazi.