2 Samuel 10:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriya aja kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Yowabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Yoabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pace.