2 Samuel 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, nakaloŵa mu mzinda. Apo Yowabu adaleka kumenyana ndi Aamoni, nabwerera ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yoabu anabwera kucokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.