2 Samuel 10:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hadadezere mfumu yao adatuma amithenga kuti akabwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate. Ndipo adafika nawo ku Helamu pamodzi ndi Sobaki, mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hadadezeri anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, iwo anapita ku Helamu motsogozedwa ndi Sobaki mkulu wa ankhondo a Hadadezeri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hadarezeri anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la cimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadarezeri anawatsogolera.