2 Samuel 10:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani, nakafika ku Helamu. Apo Asiriya adandanda kuti alimbane ndi Davide, ndipo adamenyana nayedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani ndipo anapita ku Helamu. Aaramu anayima mʼmizere yawo yankhondo kukakumana ndi Davide ndipo anamenyana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisrayeli onse, naoloka Yordano nafika ku Helemu, Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye.