2 Samuel 10:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo Davide adapha anthu apa magaleta okwanira 700, ndi ankhondo okwera pa akavalo okwanira 40,000. Adamvulaza kwambiri Sobaki, mtsogoleri wa gulu lao la ankhondo uja, kotero kuti adafera pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; Davide naphapo Aaramu apamagaleta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 700 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Davide anaphanso Sobaki mtsogoleri wawo wankhondo ndipo anafera pomwepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israyeli; Davide naphapo Aaramu apamagareta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.