2 Samuel 10:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mafumu onse amene ankatumikira Hadadezere, ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adapangana nawo za mtendere, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya nawonso adaopa kumathandizanso Aamoniwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadadezere, anaona kuti Aisraele anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisraele, nawatumikira. Chomwecho Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumu onse amene anali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, iwo anachita mtendere ndi Aisraeli ndipo anakhala pansi pawo. Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadarezeri, anaona kuti Aisrayeli anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisrayeli, nawatumikira, Comweco Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni.