2 Samuel 10:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adati, “Ndidzakhala naye mokhulupirika Hanuni, mwana wa Nahasi, monga momwe bambo wake adaandichitira zabwino.” Motero Davide adatuma atumiki kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika m'dziko la Aamoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati, Ndidzachitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wake anandichitira ine zokoma. Chomwecho Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ake kuti akamsangalatse chifukwa cha atate wake. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake. Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati, Ndidzacitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wace anandicitira ine zokoma. Comweco Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ace kuti akamsangalatse cifukwa ca atate wace. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.