2 Samuel 10:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, adatuma anthu kukalemba ntchito Asiriya a ku Beterehobu ndi a ku Zoba, ankhondo apansi okwanira 20,000. Adalembanso mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake okwanira 1,000, ndiponso anthu a ku Tobu okwanira 12,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, anakapeza ankhondo oyenda pansi aganyu okwanira 20,000 kuchokera ku Asiriya wa ku Beti Rehobu ndi Aramu-Zoba, komanso ankhondo 1,000 kwa mfumu Maaka ndiponso ankhondo 22,000 ochokera ku Tobu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Betirehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu cikwi cimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.