2 Samuel 10:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa khomo la chipata cha mzinda. Koma Asiriya a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndiponso anthu a ku Tobu ndi a ku Maaka, anali paokha ku malo opanda mitengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo polowera kuchipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene Aaramu a ku Aramu-Zoba ndi Rehobu ndi ankhondo a ku Tobu ndi Maaka anali kwa wokha ku malo wopanda mitengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo polowera kucipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.