2 Samuel 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele, naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Yowabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israele, nawandandalitsa cha kwa Aramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake, iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Yoabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israyeli, nawandandalitsa ca kwa Aramu.