2 Samuel 11:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu adamuuza Davide kuti, “Uriyatu sadapite kunyumba kwake.” Davideyo adafunsa Uriya kuti, “Kodi suja iwe wachokera ku ulendo? Nanga bwanji sudapite kunyumba kwako?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsikire kunyumba yake, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwera kuulendo? Chifukwa ninji sunatsikira kunyumba yako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsildra ku nyumba yace, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwera kuulendo? cifukwa ninji sunatsikira ku nyumba yako?