2 Samuel 11:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adaitana Uriya, nadya naye ndipo adamwa kwambiri, kotero kuti Davide adamledzeretsa. Komabe madzulo Uriya adapita kukagona pogona pake, pamodzi ndi antchito a mfumu, osapita kunyumba kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pace; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anaturuka kukagona pa kama wace pamodzi ndi anyamata a mbuye wace; koma sanatsildra ku nyumba yace.