2 Samuel 11:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ankhondo amumzindamo adatuluka nadzamenyana ndi Yowabu. Ndipo ena mwa ankhondo a Davide adaphedwa. Uriya, Muhiti uja, nayenso adaphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akumudziwo anatuluka, namenyana ndi Yowabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Muhiti anafanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akumudziwo anaturuka, namenyana ndi Yoabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Mhiti anafanso.