2 Samuel 11:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Jerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Mhiti, iyenso adafa,