2 Samuel 11:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatilaka natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatilaka naturukira kwa ife kumundako, koma tinawa gwera kufikira polowera kucipata,