2 Samuel 11:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Davide adatuma munthu kuti akafunsitse za mkaziyo. Ndipo munthuyo adamuuza kuti, “Mkazi ujatu ndi Bateseba, mwana wa Eliyamu, mwamuna wake ndi Uriya Muhiti.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu mkazi wa Uriya Mhiti?