2 Samuel 11:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Uriya adagona pakhomo pa nyumba ya mfumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake, sadapite kunyumba kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wake, osatsikira kunyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wace, osatsikira ku nyumba yace.