2 Samuel 12:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine Chauta ndikuti, ndithu ndidzakugwetsera tsoka pabanja pako pomwepo. Ndidzakuchotsera akazi ako, iweyo ukupenya, ndi kuŵapereka kwa mnzako wina, ndipo adzagona nawo akazi ako dzuŵa likuwomba mtengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzacotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa liri denene.