2 Samuel 12:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Davide adapempherera mwanayo kwa Mulungu. Adaleka kudya, nakaloŵa m'nyumba, nkukagona pansi usiku wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.