2 Samuel 12:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu a ku nyumba ya mfumu adadzaima pambali pake kuti amuutse. Koma iye adakana kuuka, ndipo sadadye nawo chakudya anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru a m'nyumba yace ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.