2 Samuel 12:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mwanayo adamwalira. Atumiki a Davide adaopa kukamuuza kuti mwanayo wafa. Adati, “Pamene mwanayo anali moyo, tinkalankhula naye Davide, koma sankatimvera. Tsono tingathe kukamuuza bwanji lero kuti mwana wafa? Mwina nkudzipweteka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwang kuti mwana wafa; sadzadzicitira coipa nanga?