2 Samuel 12:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene Davide adaona kuti atumiki ake akunong'onezana, adadziŵa kuti mwana uja wafa. Choncho adafunsa atumiki ake aja kuti, “Kodi mwana uja watisiya?” Atumikiwo adati, “Inde, watisiyadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene Davide anaona anyamata ake likunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ake, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?” Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene Davide anaona anyamata ace alikunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ace, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.