2 Samuel 12:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Davide adadzuka pansi paja, ndipo adakasamba, nadzola mafuta, nkusintha zovala zake. Tsono adakaloŵa m'nyumba ya Chauta, nakapembedza. Pambuyo pake adapita kunyumba kwake, naitanitsa chakudya. Ndipo anthu atabwera nacho, iye adadya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anayimirira. Anakasamba nadzola mafuta ndi kusintha zovala zake. Pambuyo pake anapita ku nyumba ya Yehova kukapembedza. Kenaka anapita ku nyumba kwake ndipo atapempha chakudya anamupatsa nadya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zobvala; nafika ku nyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika ku nyumba yace; ndipo powauza anamuikira cakudya, nadya iye.