2 Samuel 12:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atumiki ake aja adamufunsa kuti, “Tatifotokozerani, kodi zimene mwachitazi nzotani? Pamene mwana uja anali moyo, inu munkakana kudya. Koma pamene adamwalira, inu mudadzuka, nkuyamba kudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anyamata ake ananena naye, Ichi mwachita nchiyani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anyamata ace ananena naye, Ici mwacita nciani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya,