2 Samuel 12:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wosauka uja analibe nkanthu komwe kupatula kankhosa kakakazi kamodzi, kamene adaagula. Ndipo adakaŵeta kankhosako, mpaka kukula kali ndi iyeyo pamodzi ndi ana ake. Kankadyako chakudya chake cha munthuyo, mpaka kumamwera m'chikho chake. Kankagona pakhundu pake pa munthuyo, ndipo kankakhala ngati mwana wake wamkazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ace. Kanadyako cakudya cace ca iye yekha, kanamwera m'cikho ca iye yekha, kanagona pa cifukato cace, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wace wamkazi.