2 Samuel 12:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adaivula chisoti kumutu mfumu ya Aamoni. Chisoticho chinkalemera makilogramu agolide, ndipo pa chisotipo panali mwala wamtengowapatali. Davide adachivala chisoticho, natenga zofunkha zochuluka mumzindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachotsa korona pa mutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pa mutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mudziwo zambirimbiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacotsa korona pa mutu wa mfumu yao; kulemera kwace kunali talente wa golidi; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pa mutu wa Davide. Iye naturutsa zofunkha za mudziwo zambirimbiri.