2 Samuel 12:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo ndi mapiki ndi nkhwangwa, ndi kuŵaumbitsa njerwa. Umu ndimo m'mene adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davide adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natulutsa anthu a m'mudzimo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturutsa anthu a m'mudzimo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi nkhwangwa zacitsulo; nawapsitiriza ndi citsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kumka ku Yerusalemu.