2 Samuel 12:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina kunyumba kwa munthu wolemera uja kudafika mlendo. Munthu uja sadafune kutengako imodzi mwa nkhosa zake kapena imodzi mwa ng'ombe zake, kuti aphere mlendo wakeyo. M'malo mwake adakatenga nkhosa ya munthu wosauka uja, naphera mlendo amene adaadzamuchezera uja.” Atamva za munthuyo, Davide adapsa mtima kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing'ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zace zazing'ono ndi zazikuru, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwana wa nkhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.