2 Samuel 12:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Natani adauza Davide kuti, “Munthuyotu ndinu amene. Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ine ndidakudzoza kuti ukhale mfumu ya Aisraele, ndipo ndidakupulumutsa kwa Saulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupukumutsa m'dzanja la Saulo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Natani anati kwa Davide, “Munthuyo ndinu! Yehova, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakudzoza kukhala mfumu ya Israeli, ndipo ndinakupulumutsa mʼdzanja la Sauli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israyeli, ndinakupulumutsa m'dzanja la Sauli;