2 Samuel 12:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakupatsa banja la mbuyako, kudzanso akazi a mbuyako kuti akhale m'manja mwako, ndipo ndidakupatsanso mtundu wa Israele pamodzi ndi fuko la Yuda. Tsono zimenezi zikadakuchepera, ndikadakuwonjezera zina zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa chifukato chako, ndinakupatsanso nyumba ya Israele ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakuchepera ndikadakuonjezera zina zakutizakuti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa cifukato cako, ndinakupatsanso nyumba ya Israyeli ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakucepera ndikadakuonjezera zina zakuti zakuti.