2 Samuel 13:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisalomu mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola, dzina lake Tamara. Aminoni, mwana wina wa Davide, ankakonda Tamara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali citapita ici, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wace wokongola, dzina lace ndiye Tamara, Amnoni mwana wa Davide anamkonda iye.