2 Samuel 13:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aminoni adauza Tamara kuti, “Bwera nacho chakudya chija m'chipinda muno kuti ndidzadyere m'manja mwako.” Tamara adatenga makeke amene adaaphikawo, napita nawo kwa Aminoni, mbale wake, m'chipindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Amnoni anati kwa Tamara, Bwera naco cakudya kucipinda kuti ndikadye ca m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kucipinda kwa Amnoni mlongo wace.