2 Samuel 13:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israyeli. Cifukwa cace tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.