2 Samuel 13:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Tamarayo adati, “Iyai, mlongo wanga, kundipirikitsa chotere nkulakwa koposa zimene wandichitazi.” Koma Aminoni sadafune kumva zimene ankanena Tamarazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.” Koma anakana kumumvera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti coipa ici cakuti ulikundipitikitsa ncacikuru coposa cina cija unandicitira ine. Kama anakana kumvera.