2 Samuel 13:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Tamara adaavala deresi lalitali, la manja aatali, monga momwe ankavalira ana achinamwali a mfumu, amene sadadziŵeko amuna. Tsono mnyamata wa Aminoni uja adatulutsa Tamara, napiringidza chitseko mkaziyo atatuluka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anabvala cobvala ca mawanga mawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amabvala zotere. Ndipo mnyamata wace anamturutsa, napiringidza citseko atapita iye.