2 Samuel 13:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Tamara adadzithira phulusa kumutu, nang'amba chovala chake chachitali chimene adaavala. Ndipo adagwirira manja kumutu, namapita akulira mokweza njira yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pace, nang'amba cobvala ca mawanga mawanga cimene analikubvala, nagwira dzanja lace pamutu pace, namuka nayenda, nalira komveka.