2 Samuel 13:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye sankagona tulo chifukwa cha Tamara mlongo wake, mpaka kuchita kudwala. Tamarayo anali namwali wosadziŵa mwamuna, ndipo kunkaoneka kuti chinali chosatheka kuti Aminoniyo amchite chilichonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aminoni anapsinjikadi nayamba kudwala chifukwa cha mlongo wake Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Aminoni anachiyesa chapatali kumchitira kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Amnoni anapsinjikadi nayamba kudwala cifukwa ca mlongo wace Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Amnoni anaciyesa capatali kumcitira kanthu.