2 Samuel 13:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Abisalomu, mlongo wa Tamarayo, adamufunsa kuti, “Monga Aminoni uja wakuchimwitsa? Komabe, iwe khala phee, mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako. Zimenezi usavutike nazo.” Choncho Tamara ankakhala ngati wofedwa kunyumba kwa mlongo wake Abisalomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu mlongo wace ananena nave, Kodi mlongo wako Arononi anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale cete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usabvutika ndi cinthuci. Comweco Tamara anakhala wounguruma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wace.