2 Samuel 13:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Abisalomu sadanenepo kanthu kalikonse kabwino kapena koipa kwa Aminoni. Pakuti Abisalomuyo adaamuzonda kwambiri Aminoni chifukwa choti adaakakamiza Tamara mlongo wake kuchita naye zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisalomu sananene mawu aliwonse kwa Amnoni; abwino kapena oyipa. Iye anamuda Amunoniyo chifukwa anachititsa manyazi mlongo wake Tamara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu sanalankhula ndi Arononi cabwino kapena coipa, pakuti Abisalomu anamuda Amnoni, popeza adacepetsa mlongo wace Tamara.