2 Samuel 13:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita zaka ziŵiri zathunthu, Abisalomu anali ndi anthu ake ku ntchito yometa nkhosa ku Baala-Hazori pafupi ndi Efuremu. Tsono adaitana ana aamuna onse a mfumu kuti akakhaleko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali: nao osenga nkhosa zace ku Baalahazore pafupi pa Efraimu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu.