2 Samuel 13:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mfumu idauza Abisalomu kuti, “Iyai, mwana wanga, tisachite kupita tonse, tingakakuvutitse.” Adayesera muno ndi muno kumuumiriza, komabe Davide sadapite nao, m'malo mwake adangomdalitsa Abisalomuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, Iai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakuchulukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayankha kuti, “Ayi mwana wanga, tisapite tonsefe. Tidzakhala cholemetsa kwa iwe.” Ngakhale Abisalomu anayesetsa kuwumiriza mfumuyo, inakana kupita. Mʼmalo mwake inangomudalitsa Abisalomuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, lai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakucurukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.