2 Samuel 13:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abisalomu adati, “Chabwino, ngati inu simupita, bwanji apite nao ndi mbale wanga Aminoniyu.” Apo mfumu idafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukufuna kuti iyeyu apite nao?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.” Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Amnoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, iye apitirenji nawe?