2 Samuel 13:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abisalomu adalamula antchito ake kuti, “Muwonetsetse nthaŵi imene Aminoni akhale ataledzera ndi vinyo. Ndikakuuzani kuti, ‘Kanthani Aminoni!’ Pomwepo mumuphe. Musaope, nanga sindine ndakulamulani? Mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ace, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Amnoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Amnoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, citani camuna.