2 Samuel 13:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide, adati, “Mbuyanga, musaganize kuti ana onse a inu mfumu aphedwa, Aminoni yekha ndiye waphedwa. Zimenezi zachitika poti nzimene Abisalomu adaatsimikiziratu kale, kuyambira pa tsiku limene Aminoni adakakamiza Tamara, mlongo wa Abisalomu, kuchita naye zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonadabu mwana wa Simea mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Aminoni yekha wafa, pakuti ichi chinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anachepetsa mlongo wake Tamara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Jonadabu mwana wa Simeya mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Amnoni yekha wafa, pakuti Ici cinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anacepetsa mlongo: wace Tamara.