2 Samuel 13:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti Abisalomu atathaŵa. Tsono mlonda wapalinga poyang'ana, adangoona anthu ambiri akuchokera ku mseu wa Horonaimu, m'mbali mwa phiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa. Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ace nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwace anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.