2 Samuel 13:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atangomaliza kulankhula, adangoona ana a mfumu akubwera, ndipo anawo adayamba kubuma maliro. Pomwepo mfumuyo nayonso idalira kwambiri pamodzi ndi atumiki ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana amuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana amuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ace analira ndi kulira kwakukuru ndithu.